You are on page 1of 2

9.

Kumbukirani izi: Masiku akalembera ndi 22 July mpaka 04 August, 2013 mmadera awa:- Nsanje, Chikwawa, Mwanza, Neno ndi ma Wodi a mu mzinda wa Blantyre awa:- Mbayani, Michiru, South Lunzu, Chilomoni, ndi Blantyre City Central. Uzani anzanu za ubwino wolembetsa mayina mkaundula wa voti; Limbikitsani anzanu za kufunika kokalembetsa mkaundula nthawi yabwino; Sungani mosamala kwambiri chikalata chanu choponyera voti; MALAWI ELECTORAL COMMISSION

KULEMBETSA MAYINA MKAUNDULA WA VOTI


GAWO LOYAMBA
NSANJE CHIKWAWA MWANZA NENO MZINDA WA BLANTYRE MMA WODI AWA : Blantyre City Central Chilomoni Mbayani Michiru South Lunzu

Musagulitse kapena kupereka kwa munthu wina chikalatacho; Ziphaso zakale sizidzagwiranso ntchito pachisankho cha pa 20 May, 2014. Kalembtseni kuti mupeze chiphaso chatsopano kuti mudzathe kuvota pa 20 May, 2014.

Mukafuna kudziwa zambiri za ndondomekoyi, funsani ku:Electoral Commission Chisankho House Civic and Voter Education Department P/Bag 113 Blantyre. Tel: 01 822033/01 824769 Fax: 01 823960/01 8221449 Email: ceo@mec.org.mw

ZOFUNIKA KUDZIWA

1.0 Mau Oyamba Kulembetsa mayina mkaundula wa voti pa chisankho cha ma Khansala, a Phungu a ku nyumba ya malamulo ndi Pulezidenti ayambika pa 22 July, 2013. 2.0 Chigawo choyamba cha kalemberayu chichitika liti? Kuyambira pa 22 July mpaka pa 04 August 2013. 3.0 Kalemberayu achitika mmadera ati? Mmaboma awa:- Nsanje, Chikwawa, Mwanza, Neno ndi ma Wodi a mu mzinda wa Blantyre awa:- Mbayani, Michiru, South Lunzu, Chilomoni, ndi Blantyre City Central. 4.0 Zofunika kudziwa kwa onse wokalembetsa mkaundula wa voti ndi ziti? Kalembera wa votiyu ndi watsopano, zilibe kuti munalembetsapo mmbuyomu. Amene analembetsapo mkaundula wa voti mbuyomu ayenera kukalembetsanso mwatsopano. Kalemberayu atenga masiku khumi ndi anayi (14 days), ndipo sipadzakhala kuwonjezera masiku wolembetsa. Kalemberayu adziyamba 8 koloko mmawa kulekeza 4 koloko madzulo. Kufunika kwa kulembetsa mayina mkaundula wa voti ndi kotani? Ndi ufulu wa anthu kulembetsa mayina mkaundula wa voti kuti adzasankhe atsogoleri akumtima kwawo; Bungwe loyendetsa chisankho lidzadziwa chiwerengero cha anthu amene adzaponye voti ndipo lidzakonzekera zipangizo zokwanira; Ngati anthu salembetsa mkaundula wa voti sadzatha kuvota;
2

Ndi yekhayo yemwe adzalembetse kupikisana pachisankhochi.

mkaundula

angathe

6.0 Kodi Zomuyenereza munthu kulembetsa dzina mkaundula wa voti ndi ziti? Akwaniritse izi: Akhale mbadwa ya dziko lino; Akhale kuti wakwanitsa kapena adzakwanitsa zaka 18 pasanafike pa tsiku loponya voti pa 20 May, 2014; Akhale munthu yemwe adabadwira, kugwira ntchito kapena kuchita malonda mdera lomwe kalemberayo akuchitika; Ngati munthuyo simbadwa awonetsetse kuti wakhala mdziko muno kwa zaka zisanu ndi ziwiri (7) mosadukiza; Munthu ayenera kulembetsa dzina lake kamodzi kokha basi. Anthu akuyenera kulembetsa ku centre ya mu Wodi imene akukhala. 7.0 Kodi umboni wotsimikiza kuti munthu ndiwoyenera kulembetsa dzina mkaundula wa voti ndi uti?

5.0

Zina mwa zinthu zimene angawonetse ngati umboni ndi izi: Chiphaso choyendera ku mayiko akunja (Passport); Chikalata choyendetsera galimoto; Kalata ya msonkho; Kalata ya ukwati (mtchatho) Chitupa chakumalo omwe akugwirako ntchito; Kalata yowonetsa tsiku lomwe adabadwa; Kalata kapena chitsimikizo kuchokera kwa a mfumu; Kalata kapena chitsimikizo kuchokera kwa munthu wina yemwe adalembetsa kale mkaundula wa voti kapena kuchokera kwa mkulu woyanganira malo wolembetsera mayina mkaundula wa voti. Chiphaso chakale choponyera voti.
3

You might also like